Matthew 26:58 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Petro ankamutsatira chapatali, mpaka ku bwalo la nyumba ya mkulu wa ansembe uja. Adaloŵa m'kati, nakhala pansi pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu kuti aone m'mene zithere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Petro anamtsata kutali, kufikira kubwalo la mkulu wa ansembe, nalowamo, nakhala pansi ndi anyamata, kuti aone chimaliziro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Petro anamutsatira Iye patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Analowa nakhala pansi pamodzi ndi alonda kuti aone zotsatira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Petro anamtsata kutari, kufikira ku bwalo la mkuru wa ansembe, nalowamo, nakhala pansi ndi anyamata, kuti aone cimariziro.