Matthew 26:62 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mkulu wa ansembe onse adaimirira nafunsa Yesu kuti, “Kodi ulibe poyankha? Nzotani zimene anthuŵa akukunenezazi?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkulu wa ansembe anaimirira, nati kwa Iye, Suvomera kanthu kodi? Nchiyani ichi chimene awa akunenera Iwe?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo mkulu wa ansembe anayimirira nati kwa Yesu, “Kodi suyankha? Kodi umboni umenewu ndi otani umene anthu awa akupereka kukutsutsa Iwe?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkuru wa ansembe anaimirira, nati kwa Iye, Subvomera kanthu kodi? nciani ici cimene awa akunenera Iwe?