Matthew 26:65 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mkulu wa ansembe uja adang'amba zovala zake nati, “Kunyoza Mulungu koopsatu kumeneku! Kodi pamenepa nkufunanso mboni zina ngati? Mwadzimvera nokha kunyoza Mulungu koopsaku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo mkulu wa ansembe anang'amba zovala zake, nati, Achitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? Onani, tsopano mwamva mwanowo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zake nati, “Wanyoza Mulungu! Tifuniranji mboni zina? Taonani, tsopano mwamva mwano wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo mkuru wa ansembe 6 anang'amba zobvala zace, nati, Acitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? onani, tsopano mwamva mwanowo;