Matthew 27:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pilato ali pa mpando woweruzira milandu, mkazi wake adamtumizira mau. Adati, “Musaloŵerepo pa nkhani ya munthu wolungamayo. Inetu maloto andivuta kwambiri usiku chifukwa cha Iyeyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake anatumiza mau kwa iye, kunena, Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m'kulota ine ndasauka kwambiri chifukwa cha Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Pilato anakhala pa mpando woweruza, mkazi wake anamutumizira uthenga uwu, “Musachite kanthu ndi munthuyo, ndi wosalakwa pakuti ndavutika kwambiri lero mʼmaloto chifukwa cha munthuyo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wace anatumiza mau kwa iye, kunena, Musacite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m'kulota ine ndasauka kwambiri cifukwa ca Iye.