Matthew 27:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pilato adaŵafunsanso kuti, “Adalakwanji?” Koma anthu aja adafuula koposa kuti, “Apachikidwe pa mtanda!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anati, Chifukwa ninji? Anachita choipa chotani? Koma iwo anafuulitsa kopambana, Apachikidwe pamtanda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pilato anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani? Wachita choyipa chotani?” Koma anachita phokoso nafuwula kwambiri kuti, “Mpachikeni!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Onse anati, Apacikidwe pamtanda. Ndipo iye anati, Cifukwa ninji? anacita coipa cotani? Koma iwo anapfuulitsa kopambana, Apacikidwe pamtanda.