Matthew 27:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pilato adaona kuti sakuphulapo kanthu, ndipo kuti anthu ali pafupi kuchita chipwirikiti. Choncho adaitanitsa madzi, nkusamba m'manja pamaso pa anthu onse, nanena kuti, “Ine ndiye ndilibe kanthu pa imfa ya munthuyu. Izo nzanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndilibe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pilato ataona kuti samaphulapo kanthu, koma mʼmalo mwake chiwawa chimayambika, anatenga madzi nasamba mʼmanja mwake pamaso pa gulu la anthu. Iye anati “Ine ndilibe chifukwa ndi magazi a munthu uyu, ndipo uwu ndi udindo wanu!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndiribe kucimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha.