Matthew 27:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaluka nsangamutu yaminga naiika pamutu pake, ndipo adamgwiritsa ndodo m'dzanja lake lamanja. Kenaka adayamba kumgwadira, namaseŵera naye mwachipongwe nkumanena kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo analuka korona waminga, namveka pamutu pake, namgwiritsa bango m'dzanja lamanja lake; ndipo anagwada pansi pamaso pake, namchitira chipongwe, nati, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo kenaka analuka chipewa chaminga nachiyika pa mutu pake. Anamugwiritsa ndodo mʼdzanja lake lamanja nagwada pamaso pake namuchitira chipongwe nati, “Tikulonjereni Mfumu ya Ayuda.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo analuka korona waminga, nambveka pamutu pace, namgwiritsa bango m'dzanja lamanja lace; ndipo anagwada pansi pamaso pace, namcitira cipongwe, nati, Tikuoneni, Mfumu ya Ayuda!