Matthew 27:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yudasi, wopereka Yesu kwa adani ake uja, adaona kuti Yesu mlandu wamuipira, nthumanzi idamugwira. Tsono adakaŵabwezera akulu a ansembe ndi akulu a Ayudawo ndalama makumi atatu zasiliva zija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Yudasi yemwe anampereka Iye, poona kuti Iye anatsutsidwa kuti afe, analapa, nabweza ndalama zija zasiliva makumi atatu kwa ansembe aakulu ndi akulu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yudasi, amene anamupereka Iye, ataona kuti Yesu waweruzidwa kuti akaphedwe, anatsutsika mu mtima mwake nakabweza ndalama zamasiliva makumi atatu zija kwa akulu a ansembe ndi kwa akuluakulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Yudase yemwe anampereka Iye, poona kuti Iye anatsutsidwa kuti afe, analapa, nabweza ndalama zija zasiliva makumi atatu kwa ansembe akuru ndi akuru,