Matthew 27:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene ankatuluka mumzindamo, adakumana ndi munthu wina, dzina lake Simoni, wa ku Kirene. Tsono asilikali aja adamkakamiza kuti asenze mtanda wa Yesu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakutuluka pao anapeza munthu wa ku Kirene, dzina lake Simoni, namkakamiza iye kuti anyamule mtanda wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene gululi linkatuluka ndi Yesu, anakumana ndi munthu wochokera ku Kurene dzina lake Simoni ndipo anamuwumiriza kunyamula mtanda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakuturukapao anapeza munthu wa ku Kurene, dzina lace Simoni, namkangamiza iye kuti anyamule mtanda wace.