Matthew 27:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankanena kuti, “Iwe, suja unkati, ‘Ndidzapasula Nyumba ya Mulungu nkuimanganso pa masiku atatu?’ Ngati ndiwedi Mwana wa Mulungu tadzipulumutsatu nkutsika pamtandapo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nati, Nanga Iwe, wopasula Kachisi, ndi kummanganso masiku atatu, tadzipulumutsa wekha; ngati uli Mwana wa Mulungu, tatsika pamtandapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anati, “Iwe amene ungapasule Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanga masiku atatu, dzipulumutse wekha! Tsika pa mtandapo ngati ndiwe Mwana wa Mulungu!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nati, Nanga 2 Iwe, wopasula Kacisi, ndi kummanganso masiku atatu, tadzipulumutsa wekha; 3 ngati uli Mwana wa Mulungu, tatsika pamtandapo.