Matthew 27:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akulu a ansembe aja adatola ndalamazo nati, “Malamulo athu satilola kuika ndalamazi m'bokosi la chuma cha m'Nyumba ya Mulungu, popeza kuti ndi za magazi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ansembe aakulu anatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziika m'chosonkhera ndalama za Mulungu, chifukwa ndizo mtengo wa mwazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akulu a ansembe anatola ndalamazo nati, “Sikololedwa ndi lamulo kuti ndalamazi tiziyike mosungira chuma cha Mulungu, popeza ndi ndalama za magazi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ansembe akuru anatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziika m'cosonkhera ndalama za Mulungu, cifukwa ndizo mtengo wa mwazi.