Matthew 27:64 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mulamule kuti azilondapo pamanda pake mpaka mkucha. Tikuwopa kuti ophunzira ake angadzabwere nkudzaba mtembo wake, kenaka namadzauza anthu kuti ‘Iye uja wauka kwa akufa.’ Apo kunyenga kotsirizaku kudzakhala koipa zedi kupambana koyamba kuja.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake mulamule kuti asindikize pamandapo, kufikira tsiku lachitatulo, kuti kapena ophunzira ake angadze, nadzamuba Iye, nadzanena kwa anthu, kuti Iye anauka kwa akufa: ndipo chinyengo chomaliza chidzaposa choyambacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho lamulirani kuti manda ake atetezedwe mpaka pa tsiku lachitatu. Chifukwa tikapanda kutero, ophunzira ake angabwere kudzaba mtembo wake ndipo angawuze anthu kuti waukitsidwa kwa akufa. Ndipo chinyengo chomalizachi chidzakhala choyipa kwambiri kusiyana ndi choyamba chija.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace mulamule kuti asindikize pamandapo, kufikira tsiku lacitatulo, kuti kapena ophunzira ace angadze, nadzamuba Iye, nadzanena kwa anthu, kuti Iye anauka kwa akufa: ndipo cinyengo comariza cidzaposa coyambaco.