Matthew 28:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku la Sabata ya Ayuda litapita, Maria wa ku Magadala ndi Maria wina uja adabwera mbandakucha pa tsiku lotsatira Sabatalo, kudzaona manda aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo popita tsiku la Sabata, mbandakucha, tsiku lakuyamba la sabata, anadza Maria wa Magadala, ndi Maria winayo, kudzaona manda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Litapita tsiku la Sabata, mmawa wa tsiku loyamba la Sabata, Mariya wa ku Magadala ndi Mariya wina anapita kukaona manda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo popita dzuwa la Sabata, mbanda kuca, tsiku lakuyamba la sabata, anadza Mariya wa Magadala, ndi Mariya winayo, kudzaona manda.