Matthew 3:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ine ndimakubatizani ndi madzi, kusonyeza kuti mwatembenuka mtima. Koma amene akubwera pambuyo panga ndi wamphamvu kuposa ine. Ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kunyamula nsapato zake. Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndiponso m'moto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine ndikubatizani ndi madzi kusonyeza kutembenuka mtima. Koma pambuyo panga akubwera wina amene ali ndi mphamvu kuposa ine, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani ndi Mzimu Woyera ndi moto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zace: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto: