Matthew 3:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chopetera chake chili m'manja kuti apete tirigu wake. Tsono adzathira tirigu m'nkhokwe, koma mankhusu adzaŵatentha m'moto wosazimika.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼdzanja lake muli chopetera ndipo adzayeretsa popunthirapo pake nadzathira tirigu wake mʼnkhokwe ndi kutentha zotsalira zonse ndi moto wosazima.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
couluzira cace ciri m'dzanja lace, ndipo adzayeretsa padwale pace; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wace m'ciruli, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.