Matthew 3:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankaona Ayuda ambiri a m'gulu la Afarisi ndi la Asaduki akubwera kuti iye aŵabatize. Tsono iyeyo ankati, “Ana a njoka inu, adakuchenjezani ndani kuti muthaŵe chilango cha Mulungu chikudzachi?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye pakuona ambiri a Afarisi ndi a Asaduki akudza ku ubatizo wake, anati kwa iwo, Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthawa mkwiyo ulinkudza?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iye ataona Afarisi ndi Asaduki ambiri akubwera kumene ankabatiza, anawawuza kuti, “Ana a njoka inu! Ndani anakuchenjezani kuthawa mkwiyo umene ukubwera?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye pakuona ambiri a Afarisi ndi a Asaduki akudza ku ubatizo wace, anati kwa iwo, Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthawa mkwiyo ulinkudza?