Matthew 4:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu akuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, adaona anthu aŵiri pachibale pao: Simoni wotchedwa Petro, ndi mbale wake Andrea, akuponya khoka m'nyanjamo, popeza kuti anali asodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andrea, mbale wake, analikuponya khoka m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wotchedwa Petro ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja popeza anali asodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andreya, mbale wace, analikuponya psasa m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba.