Matthew 4:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atapitirira pamenepo, Yesu adaona enanso aŵiri pachibale pao: Yakobe ndi Yohane, ana a Zebedeo. Iwo anali m'chombo pamodzi ndi bambo waoyo, akukonza makoka ao, Yesu nkuŵaitana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo popitirirapo Iye anaona abale ena awiri, Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake, m'ngalawa, pamodzi ndi Zebedeo atate wao, analikusoka makoka ao; ndipo anaitana iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atapita patsogolo, anaona abale ena awiri, Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo. Iwowa anali mʼbwato ndi abambo awo, Zebedayo, akukonza makoka awo ndipo Yesu anawayitana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo popitirirapo Iye anaona abale ena awiri, Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace, m'ngalawa, pamodzi ndi Zebedayo atate wao, analikusoka makoka ao; ndipo anaitana iwo.