Matthew 4:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, mudziponye pansi. Paja Malembo akuti, “ ‘Mulungu adzalamula angelo ake kuti akusamaleni, iwo adzakunyamulani m'manja mwao, kuti mapazi anu angapweteke pa miyala.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti, Adzalamula angelo ake za iwe, ndipo pa manja ao adzakunyamula iwe, ungagunde konse phazi lako pamwala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, dziponyeni nokha pansi. Pakuti kwalembedwa: “ ‘Adzalamulira angelo ake za iwe, ndipo adzakunyamula ndi manja awo kuti phazi lako lisagunde pa mwala.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti, Adzauza angelo ace za iwe, Ndipo pa manja ao adzakunyamulaiwe, Ungagunde konse phazi lako pamwala.