Matthew 5:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunyengezerani zoipa zamitundumitundu chifukwa cha Ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, kukunenerani zoyipa zilizonse ndi kukunamizirani chifukwa cha Ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa ziri zonse cifukwa ca Ine.