Matthew 5:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithu ndikunenetsa kuti thambo ndi dziko lapansi zisanathe, sipadzachoka kalemba nkakang'ono komwe kapena kankhodolera pa Malamulowo, mpaka zonse zitachitika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kake kamodzi sikadzachokera kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikukuwuzani zoonadi kuti, kufikira kutha kwa thambo ndi dziko lapansi, chilichonse chimene chinalembedwa mʼmalamulo, ngakhale kalemba kakangʼonongʼono, chidzakwaniritsidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kace kamodzi sikadzaeokera kucilamulo, kufikira zitacitidwa zonse.