Matthew 5:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho aliyense wonyozera limodzi mwa malamulo ameneŵa, ngakhale laling'ono chotani, nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamng'ono ndithu mu Ufumu wakumwamba. Koma aliyense amene amaŵatsata nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamkulu mu Ufumu wakumwamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake yense wakumasula limodzi la malamulo amenewa ang'onong'ono, nadzaphunzitsa anthu chomwecho, adzatchulidwa wamng'onong'ono mu Ufumu wa Kumwamba; koma yense wakuchita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzatchulidwa wamkulu mu Ufumu wa Kumwamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chake aliyense amene aphwanya limodzi la malamulowa ngakhale lalingʼonongʼono ndi kuphunzitsa ena kuti achite chimodzimodzi, adzakhala wotsirizira mu ufumu wakumwamba, koma aliyense amene achita ndi kuphunzitsa malamulo awa adzakhala wamkulu mu ufumu wakumwamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace yense wakumasula limodzi la malangizo amenewa ang'onong'ono, nadzaphunzitsa anthu comweco, adzachulidwa wamng'onong'ono mu Ufumu wa Kumwamba; koma yense wakucita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzachulidwa wamkuru mu Ufumu wa Kumwamba.