Matthew 5:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense wopsera mtima mbale wake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu. Aliyense wonena mnzake kuti, ‘Wopandapake iwe,’ adzayenera kuzengedwera ku Bwalo Lapamwamba. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru,’ adzayenera kukaponyedwa ku moto wa Gehena.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wokwiyira mʼbale wake adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene wonena mʼbale wake kuti, ‘Ndiwe wopanda phindu,’ adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu lalikulu. Ndipo aliyense amene anganene mnzake ‘wopandapake’ adzatengeredwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene angamunene mnzake kuti, ‘Chitsiru iwe,’ adzaponyedwa ku gehena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wace wopanda cifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wace, Wopanda pace iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akuru: koma amene adzati, Citsiru iwe: adzakhala wopalamula gehena wamoto.