Matthew 5:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Uziyanjana msanga ndi mnzako wamlandu, mukali pa njira yopita ku bwalo lamilandu, kuwopa kuti angakakupereke kwa woweruza, woweruzayo angakakupereke kwa msilikali, ndipo msilikaliyo angakakuponye m'ndende.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Fulumira kuyanjana ndi mnzako wamlandu, pamene uli naye panjira; kapena mnzako wamlandu angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, nuponyedwe iwe m'nyumba yandende.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Fulumira kuyanjana ndi mnzako amene unamulakwira nthawi ya milandu isanafike chifukwa angakupereke kwa oweruza amene angakupereke kwa mlonda ndipo mlondayo angakutsekere mʼndende.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Fulumira kuyanjana ndi mnzako wamlandu, pamene uli naye panjira; kapena mnzako wamlandu angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angapereke iwe kwa msilikari, nuponyedwe iwe m'nyumba yandende.