Matthew 5:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muleke nkulumbira komwe. Usalumbire kuti, ‘Kumwambadi!’ Paja Kumwamba kuli mpando waufumu wa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma Ine ndinena kwa inu, Musalumbire konse, kapena kutchula Kumwamba, chifukwa kuli chimpando cha Mulungu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndikuwuzani kuti musalumbire ndi pangʼono pomwe kutchula kumwamba chifukwa kuli mpando waufumu wa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma Ine ndinena kwa inu, 6 Musalumbire konse, kapena kuchula Kumwamba, cifukwa kuli cimpando ca Mulungu;