Matthew 5:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usalumbire kuti, ‘Pali dziko lapansi!’ Paja dziko lapansi ndi chopondapo mapazi ake. Usalumbire kuti, ‘Pali Yerusalemu!’ Paja Yerusalemu ndi mzinda wa Mfumu yaikulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa lili popondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa kuli mzinda wa Mfumu yaikulukulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa ndi chopondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa ndi mzinda wa mfumu yayikulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
7 kapena kuchula dziko lapansi, cifukwa liri popondapo mapazi ace; kapena kuchula Yerusalemu, cifukwa kuli mzinda wa Mfumu yaikurukuru.