Matthew 5:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usalumbire ngakhale pa mutu wako, pakuti sungathe kusandulitsa ndi tsitsi limodzi lomwe kuti likhale loyera kapena lakuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena usalumbire kumutu wako, chifukwa sungathe kuliyeretsa mbu kapena kulidetsa bii tsitsi limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo musalumbire ndi mutu wanu chifukwa simungathe kuyeretsa ngakhale kudetsa tsitsi limodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
8 Kapena usalumbire ku mutu wako, cifukwa sungathe kuliyeretsa mbu kapena kulidetsa bii tsitsi limodzi.