Matthew 5:45 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukatero mudzakhaladi ana a Atate anu amene ali Kumwamba. Paja Iwo amaŵalitsa dzuŵa lao pa anthu abwino ndi pa anthu oipa omwe, ndipo amagwetsera mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; chifukwa Iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuti mukhale ana a Atate anu akumwamba, amene awalitsa dzuwa lake pa oyipa ndi pa abwino, nagwetsa mvula pa olungama ndi pa osalungama.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; cifukwa Iye amakwezera dzuwa lace pa oipa ndi pa abwino, namabvumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.