Matthew 5:46 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mungalandire mphotho yanji? Kodi suja ngakhale okhometsa msonkho amachita chimodzimodzi?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati mukonda amene akukondani inu, mudzapeza mphotho yanji? Kodi ngakhale amisonkho sachita chimodzimodzi?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa kuti 17 ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? kodi angakhale amisonkho sacita comweco?