Matthew 6:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pamene mukusala zakudya, musamaonetsa nkhope zachisoni monga amachitira anthu achiphamaso aja. Iwo amaipitsa nkhope kuti anthu aone kuti akusala zakudya. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yachisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alimkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pamene mukusala kudya, musaonetse nkhope yachisoni monga achita achiphamaso, pakuti iwo amasintha nkhope zawo kuonetsa anthu kuti akusala kudya. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yacisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alimkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.