Matthew 6:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ngati maso ako sali bwino, m'thupi mwako monse mumakhala mdima. Tsono ngati kuŵala kumene kuli mwa iwe kusanduka mdima, mdima wakewo ndi wochita kuti goo!
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati diso lako lili loipa, thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa. Chifukwa chake ngati kuwala kumene kuli mwa inu kuli mdima, mdimawo ndi waukulu ndithu!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati maso ako sali bwino, thupi lako lonse lidzakhala mu mdima. Koma ngati kuwala kuli mwa iwe ndi mdima, ndiye kuti mdimawo ndi waukulu bwanji!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati diso lako liri loipa, thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa. Cifukwa cace ngati kuwala kumene kuli mwa inu kuli mdima, mdimawo ndi waukuru ndithu!