Matthew 6:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati Mulungu aveka chotero udzu wa kuthengo, ukhala lero, ndi mawa uponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati umu ndi mmene Mulungu avekera udzu wa kutchire umene ulipo lero ndipo mawa uponyedwa ku moto, kodi sadzakuvekani koposa? Aa! Inu a chikhulupiriro chochepa!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati Mulungu abveka cotero maudzu a kuthengo, akhala lero, ndi mawa oponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono?