Matthew 6:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pamene mukupemphera, musachite monga anthu achiphamaso aja. Iwowo amakonda kuimirira ndi kupemphera m'nyumba zamapemphero ndi pa mphambano za miseu yam'mizinda. Amachita zimenezi kuti anthu aŵaone. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pamene mupemphera, musakhale ngati achiphamaso, chifukwa iwo amakonda kupemphera choyimirira mʼmasunagoge ndi pa mphambano za mʼmisewu kuti anthu awaone. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; cifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.