Matthew 6:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pamene mukupemphera, musamangobwerezabwereza mau monga amachitira anthu akunja. Iwowo amayesa kuti akachulukitsa mau choncho, ndiye pamene Mulungu aŵamvere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo popemphera musabwerezebwereze chabe iai, monga amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhulalankhula kwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo pamene mukupemphera, musamabwerezabwereza monga akunja, pakuti iwo amaganiza kuti adzamveka chifukwa chochulutsa mawu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo popemphera musabwereze-bwereze cabe iai, monga amacita anthu akunja, cifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhula-lankhula kwao.