Matthew 7:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma chipata ndi chopapatiza ndi msewu ndi waungʼono umene utsogolera anthu ku moyo wosatha ndipo ndi owerengeka okha amene ayipeza njirayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti cipata ciri copapatiza, ndi icepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akucipeza cimeneco ali owerengeka.