Matthew 7:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Chenjerani nawo aneneri onyenga. Amabwera kwa inu atavala zikopa zankhosa, koma mʼkati mwawo ali mimbulu yolusa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zobvala zankhosa, koma m'kati mwao ali afisi alusa.