Matthew 7:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Musamapatsa agalu zinthu zopatulika, kapena kuponyera nkhumba ngale zamtengowapatali, kuwopa kuti zingazipondereze, kenaka nkukutembenukirani ndi kukukadzulani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Musapatse agalu zinthu zopatulika; kapena musaponyere nkhumba ngale zanu. Pakuti ngati mutero, zidzaziponda ndipo pomwepo zidzakutembenukirani ndi kukudulani nthulinthuli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamapatsa copatulikaco kwa agaru, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.