Matthew 8:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithu ndikunenetsa kuti ambiri adzabwera kuchokera kuvuma ndi kuzambwe nadzakhala nao pa phwando mu Ufumu wakumwamba pamodzi ndi Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinena ndi inu, kuti ambiri a kum'mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, mu Ufumu wa Kumwamba;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikuwuzani kuti ambiri adzabwera kuchokera kummawa ndi kumadzulo, nadzakhala nawo pa phwando pamodzi ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo mu ufumu wakumwamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinena ndi inu, kuti ambiri a kum'mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, mu Ufumu wa Kumwamba;