Matthew 8:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Madzulo amenewo, anthu adabwera kwa Yesu ndi anzao ambiri ogwidwa ndi mizimu yoipa. Yesu adaitulutsa mizimuyo ndi mau chabe, ndipo onse amene ankadwala adaŵachiritsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda; ndipo Iye anatulutsa mizimuyo ndi mau, nachiritsa akudwala onse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Itafika nthawi yamadzulo, anthu anabweretsa kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda ndipo anatulutsa ziwandazo ndi mawu okha, nachiritsa odwala onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi mizimu yoipa; ndipo Iye anaturutsa mizimuyo ndi mau, naciritsa akudwala onse;