Matthew 8:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuchita mantha, inu anthu a chikhulupiriro chochepa?” Atatero adaimirira nkudzudzula mphepoyo ndi nyanjayo, kenaka padagwa bata lalikulu ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang'ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawayankha kuti, “Inu achikhulupiriro chochepa, chifukwa chiyani mukuchita mantha?” Ndipo anayimirira nadzudzula mphepoyo ndi mafunde ndipo panali bata lalikulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang'ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikuru.