Matthew 8:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu atafika ku tsidya la nyanja, ku dera la Agadara, anthu aŵiri ogwidwa ndi mizimu yoipa adadzakumana naye kuchokera ku manda. Anali aukali kwambiri, kotero kuti panalibe munthu ndi mmodzi yemwe wotha kudzera njira imeneyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pofika Iye kutsidya lina, kudziko la Agadara, anakomana naye awiri ogwidwa ndi ziwanda, akutuluka kumanda, aukali ndithu, kotero kuti sangathe kupitapo munthu pa njira imeneyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo atafika ku mbali ina ya dera la Gadara, anakumana ndi anthu awiri ogwidwa ndi ziwanda akuchokera ku manda. Iwowa anali woopsa kwambiri kotero kuti panalibe munthu akanatha kudzera njira imeneyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pofika Iye ku tsidya lina, ku dziko la Agadara, anakomana naye awiri ogwidwa ndi ziwanda, akuturuka kumanda, aukali ndithu, kotero kuti sangathe kupitapa munthu pa njira imeneyo.