Matthew 8:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwadzidzidzi anthuwo adayamba kufuula kuti, “Kodi takuputani chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwera kuno kudzatizunza nthaŵi isanakwane?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo onani, anafuula nati, Tili nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siinafike?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iwo anafuwulira kwa Yesu nati, “Mukufuna chiyani kwa ife, Inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwera kuno kudzatizunza nthawi yake isanafike?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo onani, anapfuula nati, Tiri nanu ciani, inu Mwana wa Mulungu? mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yace siinafike?