Matthew 8:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adaiwuza kuti, “Chabwino, pitani!” Iyo idatuluka nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja mpaka kufera m'madzimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iyo, Mukani. Ndipo inatuluka, nimuka, kukalowa m'nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse linathamangira kunsi kuphompho m'nyanjamo, ndipo linafa m'madzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati kwa ziwandazo, “Pitani!” Ndipo pamenepo zinatuluka ndi kukalowa mʼnkhumbazo ndipo nkhumba zonse zinathamangira mʼnyanja ndi kufera momwemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iyo, Mukani. Ndipo inaturuka, nimuka, kukalowa m'nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse linathamangira kunsi kuphompho m'nyanjamo, ndipo linafa m'madzi.