Matthew 8:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inetu ndili ndi akuluakulu ondilamulira, komanso ndili ndi asilikali amene ineyo ndimaŵalamulira. Ndimati ndikauza wina kuti, ‘Pita,’ amapitadi. Ndikauzanso wina kuti, ‘Bwera,’ amabweradi. Ndipo ndikauza kapolo wanga kuti, ‘Chita chakuti,’ amachitadi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti inenso ndili munthu wakumvera ulamuliro, ndili nao asilikali akundimvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndi kwa kapolo wanga, Chita ichi, nachita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti inenso ndili pansi pa ulamuliro ndipo ndili ndi asilikali amene ndiwalamulira. Ndikalamulira mmodzi kuti, ‘Pita,’ amapita; ndi kwa wina kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikawuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ iye amachita.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti inenso ndiri munthu wakumvera ulamuliro, ndiri nao asilikari akundimvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndi kwa kapolo wanga, Cita ici, nacita.