Matthew 9:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ophunzira a Yohane Mbatizi adabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Kodi bwanji ife ndi Afarisi timasala zakudya kaŵirikaŵiri, pamene ophunzira anu sasala nkomwe?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo anadza kwa Iye ophunzira ake a Yohane, nati, Chifukwa ninji ife ndi Afarisi tisala kudya kawirikawiri, koma ophunzira anu sasala?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ophunzira a Yohane anabwera namufunsa Iye kuti, “Bwanji ife ndi Afarisi timasala kudya koma ophunzira anu sasala kudya?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo anadza kwa Iye ophunzira ace a Yohane, nati, Cifukwa ninji ife ndi Afarisi tisala kudya kawiri kawiri, koma ophunzira anu sasala?