Matthew 9:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yesu ankakamba zimenezi, munthu wina wamkulu adadzamgwadira nati, “Mwana wanga wamkazi wamwalira tsopano apa. Chonde bwerani mudzamsanjike manja, kuti akhale ndi moyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mene Iye analikulankhula nao zinthu zimenezo, onani, anadza munthu mkulu, namgwadira Iye, nanena, Wamwalira tsopanoli mwana wanga wamkazi, komatu mudze muike dzanja lanu pa iye, ndipo adzakhala ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene ankanena zimenezi, mkulu wa sunagoge anabwera namugwadira Iye nati, “Mwana wanga wamkazi wamwalira posachedwapa koma tiyeni mukasanjike dzanja lanu pa iye ndipo adzakhala ndi moyo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mene Iye analikulankhula nao zinthu zimenezo, onani, anadza munthu mkuru, namgwadira Iye, nanena, Wamwalira tsopanolimwana wanga wamkazi, komatu mudze muike dzanja lanu pa iye, ndipo adzakhala ndi moyo.