Matthew 9:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri. Iyeyu adafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza mphonje ya chovala chake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo onani, mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chofunda chake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Panali mayi wina amene ankadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri ndipo anadza mʼmbuyo mwake nakhudza mkanjo wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo onani, mkazi, anali ndi nthenda yacidwalire zaka khumi ndi ziwiri, anadza pambuyo pace, nakhudza mphonje ya copfundacace;