Matthew 9:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu ataloŵa m'nyumba, akhungu aja adadzampeza, Iye nkuŵafunsa kuti, “Kodi mukukhulupirira kuti ndingathe kuchita zimenezi?” Iwo adati, “Inde, Ambuye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atalowa mʼnyumba, amuna awiri osaonawo anabwera kwa Iye ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mukhulupirira kuti ndikhoza kukuchiritsani?” Iwo anayankha kuti, “Inde Ambuye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kucita ici? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye.