Matthew 9:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene adaona makamu a anthu, adaŵamvera chifundo, chifukwa iwo anali olema ndi ovutika ngati nkhosa zopanda mbusa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ataona maguluwo, anagwidwa ndi chisoni chifukwa anali ozunzika ndi osowa chithandizo ngati nkhosa zopanda mʼbusa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi cisoni cifukwa ca iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.