Matthew 9:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa Munthu ali nazo mphamvu pansi pano zokhululukira machimo, onani.” Pamenepo adauza wofa ziwalo uja kuti, “Iwe, dzuka, tenga machira ako, uzipita kumudzi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvu Mwana wa Munthu pansi pano za kukhululukira machimo (pomwepo ananena kwa wodwalayo), Tanyamuka, nutenge mphasa yako, numuke kunyumba kwako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko wokhululuka machimo, pamenepo anati kwa wakufa ziwaloyo, ‘Imirira, tenga mphasa yako kazipita kwanu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvu Mwana wa munthu pansi pano za kukhululukira macimo (pomwepo ananena kwa wodwalayo), Tanyamuka, nutenge chika lako, numuke kunyumba kwako.